Maskal - Ndiwe Wanga lyrics
rate me<b>Ndiwe Wanga</b> by <i>Maskal</i><br />
Verse; 1
Pazachikondi chako dziwa ine ndi mboni
Sindinalakelake kupita ku Joni
Chikondi cha iwe ndi ine sicham'mafoni
Nchifukwa sindinapite ku bank kukatenga loan
Chikondi chathu chobeba chanoninoni
Umandizula moyo ukapereka moni
Umandikumbutsa za kwathu kumangoni
Ndakondwa umadziwa kuti ine ndi m'goni
Chorus*2
Ndiwe wanga ndiwe kuwala kwanga
Ndiwe wanga ndiwe nyenyezi yanga
Ndiwe wanga ndiwe wanga ndiwe wapamtima wanga
Ndiwe wanga ndiwe wanga nyenyezi yanga
Ndiwe wanga ndiwe kuwala kwanga
Verse; 2
Ndikakha pansi ndimadziwa ndiri ndi mzanga
Kuyenda limodzi tifanana mawanga
Amandinena ati ndiri nyanga
Asatilongoze monga ichita nkhanga
Ndithudi ndilonjeza ndzakutengela kunyanja
Nthawi imeneyo tikukonzekera banja
Ona ambiri akutiombera m'manja
Mpakana wena kutimangira nsanja
(Back to chorus)
Verse; 3
Chikondi chathu chansangala sizachisoni
Ena amasangalala akatipatsa moni
Unasiya amabenzi onse ndimalinkoni
Amatithila madzi ndikumaimba horn
Akamaditsa baby, Samamvetsa baby
Ngati andale baby, Ali pa njale baby
Zimawawawa baby, Kuiwala mawa baby
Ngati moyenda baby, Ife tikuyenda baby!, Hee!
(Back to chorus till the end)